NJIRA ZA KACHOTSEDWE KA UCHI MU MALESA
NJIRA ZA KACHOTSEDWE KA UCHI MU MALESA
1. Kulola uchi kodotha / kukha wokha kuchokera mu zisa (Dripping method)
Ku Malawi kuno njira imene alimi anjuchi ambiri amagwiritsa ntchito posefa uchi ndi yogwiritsa ntchito nsalu pa ndowa kapena chidebe.
Zoyenera kutsata kapena kukhala nazo posefa uchi ndi izi:
- Nsalu yoyera yabwino (waster)
- Mipeni
- Sapuni
- Ndowa ndi zigubu zokwanira
- Mphira ndi magorovesi.
Ndondomeko yake
- Onenetsetsani kuti malo anu ndiosamalika
- Pakhale madzi okwanira
- Ikani nsalu ndi kumanga pakamwa pa ndowa kapena chidebe
- Tengani zisa ndi kuyika pamwamba pa nsalu imene mwamanga pa ndowa kapena pachidebe kuti uchi uzidontha kapena kuwukha ndi kumagwera mu ndowa kapena muchidebe
- Madzi auchi akatha kudontha chotsani zisa ndi kuzisamalira
- Ndowa kapena chidebe chimene mwagwiritsira ntchito chitsekedwe ndikuikidwa pa malo abwino ozizira.
Uchi wake umakhala wabwino kwambiri koma uchi wina umakhalira mumalesa komanso ndi njira yotenga nthawi.
2. Kufinya zisa / Pressing method
- Iyi ndi njira yomwe imagwiritsidwa ntchito pofinya uchi koma ndiyokwera mtengo.
- Uchi wochuluka umapezeka chifukwa sukhalira kumalesa/mzisa komanso ndi njira ya changu.
Palinso makina amene alimi a njuchi amagwiritsa ntchito pofinyauchi.