ZINTHU ZOPANGIDWA KUCHOKERA KU NJUCHI
ZINTHU ZOPANGIDWA KUCHOKERA KU NJUCHI
Uchi
Uchi ndi chinthu choyamba komanso chenicheni chimene mlimi amapeza ku njuchi. Uchi ndi chakudya komanso umagwiritsidwa ntchito m’mafakitale pokonza zakudya ndi zakumwa zosiyanasiyana.
Sera (Wax)
Sera amapangidwa kuchokera kumalesa a njuchi. Sera amagwiritsidwa ntchito popangira zinthu zosiyanasiyana monga makandulo, mafuta odzola a madzimadzi, zopaka m’milomo kapena muzala, mankhwala opakira pa simenti (flour polish), mipando komanso nsapato. Paulimi wanjuchi, alimi amagwiritsira ntchito popaka ming’oma yawo kuti njuchi zilowe msanga.
Phula
Njuchi zimapanga phula kuchokera kumitengo pomwe pakhapidwa. Ntchito yaphula ndimonga kutseka mipata ming’oma komanso limachiza matenda osiyanasiyana monga mphenga, fungo la mkamwa, zilonda zapakhosi ndi mkamwa.