ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

KHUKU ZA MAZIRA NDI ZA NYAMA

NKHUKU ZA MAZIRA NDI ZA NYAMA

Kawirikawiri nkhuku za mitundu iyi ndi zomwe zimayikira mazira ochuluka kapena kukhala ndi nyama yochuluka.

1. Kulera anapiye

Chikuta

Anapiye akatuluka mmashini amafunika kufikira malo otentha kuti asafe ndi mphepo.

Kukonzekera Kulera Anapiye

  • Sesani mkhola ndikukoloperamo mankhwala a mtundu wa “disinfectant”
  • Sanjikani njerwa ndikuikapo mbaula yonyeka bwino kuti mu chipinda mutenthere bwino
  • Ikani utuchi ochuluka bwino m’khola
  • Ikani madzi muzomwera zabwino tianapiye tikabwera

Chomwera madzi

  • Kenako tipatseni chakudya cha chick mash.

Mmene tiana timakhalira molingana ndi kutentha kwa mkhola mu chikuta

Kutentha koyenera

Kutentha kwambiri

Kuzizira kwambiri

Mphepo yozizira ikulowa kwambiri

2. Khola la nkhuku za mazira ndi nyama

Mangani khola la pansi la nkhuku za mtundu wa zamazira ndi zanyama linafotokonzeredwa pa gawo la nkhuku zamakolo

Mlingo wa malo okwanira nkhuku mkhola

Pamene tikumanga khola tiyenera kulingalira za mtundu wa nkhuku umene tikufuna kuweta tisamange khola chisawawa.

3. Chakudya

Nkhuku zamsinkhu osiyana zimadyanso chakudya chosiyana monga:

Zamazira

Nkhuku Zanyama

Madzi

Ikani madzi mukhola okwanira bwino ndiponso a ukhondo, ikani zomwera zokwanira ndipo sinthani madzi ngati awonongeka kapena atentha. 

Share this Doc