KUSANKHA MALO NDI ZIPANGIZO ZOMANGIRA KHOLA
KUSANKHA MALO NDI ZIPANGIZO ZOMANGIRA KHOLA
- Sankhani malo otetezedwa ku mbava ndi nyama zolusa
- Malo omanga khola akhale mbali yomwe ikupita mphepo kupewa fungo kuti lisalowe mnyumba yogona
- Mangani malo opanda lowe
- Khola lisatalikire kwambiri kuchokera pa nyumba yogona anthu
- Lambulani tchire lonse kuzungulira khola malo okwana mamita atatu kuopetsa zirombo zogwila nkhuku.
Zipangizo zomangira Khola
Gwiritsani ntchito zipangizo zomangira khola zopezeka mosavuta monga:
- Mitengo
- Njerwa
- Bango
- Dothi
- Udzu, malata ndi zina zotero.