MAKOLA ANKHUKU
MAKOLA ANKHUKU
Makola ankhuku za makolo alipo a mitundu iwiri omwe ndi:
Lam’mwamba
Iri limamangidwa ndi zipangizo zopezeka mosabvuta monga nsungwi, bango
Khola likhale pa mlingo wa 1.0m kuchokera pansi
Lapansi
- Mangani khola molingana ndi kuchuluka kwa nkhuku zanu, mwachitsanzo nkhuku 10 mpaka 15 zimafunika khola lotalika mita imodzi mbali zonse
- Folerani denga la khola ndi udzu kapena malata kuti m’khola muzikhala mouma nthawi zonse
- Ikani utuchi m’khola kuti nkhuku zizigona pabwino
- Konzani malo abwino oyikira nkhuku kuti mazira asasweke komanso azikhala aukhondo
- Onetsetsani kuti m’khola ndi mwaukhondo nthawi zonse.