ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

MATENDA A NKHUKU NDI ZOYENERA KUCHITA

MATENDA A NKHUKU NDI ZOYENERA KUCHITA

Chitopa

  • Matenda a chitopa timayambitsa ndi tizirombo ta mtundu wa vayilasi
  • Chitopa chimagwira nkhuku ya msikhu uliwonse
  • Matendawa alibe makhwala ochiza
  • Chofunika ndikuteteza nkhuku zisanadwale

Zizindikiro za Chitopa

  • Nkhuku imatentha thupi
  • Nkhuku siyimadya
  • Nkhuku imapuma mobanika
  • Nkhuku imapinda khosi
  • Nkhuku zimachita chitosi chobiriwira
  • Nkhuku imatsokomola/kukhosomola
  • Nkhuku imafundira mapiko
  • Nkhuku zimafa zambiri ndipo nthawi zina zimafa zonse.





Zoyenera kuchita poteteza

  • Chotsani nkhuku zimene zasonyeza zizindikiro za chitopa ndi kuziyika pazokha
  • Tetezani nkhuku zanu zisanadwale pozipatsa katemera
  • Musalore anthu osiyanasiyana kulowa mu khola la nkhuku ndipo onetsetsani kuti olowa mkhola aponde madzi a mankhwala a mtundu wa (disinfectant) opha tizirombo
  • Perekani katemera wotchedwa Lasota kapena I2 pakatha miyezi itatu kapena inayi iri yonse kuti muteteze nkhuku ku matenda a chitopa.

Gumboro

  • Matenda a Gumboro timayambitsa ndi tizirombo tamtundu wa vayilasi
  • Amagwira nkhuku za msinkhu woyambira tsiku limodzi mpaka masabata 8
  • Matendawa amafala kudzera mu mumphweya, fumbi, zitosi, ziwiya ndi kusuntha nkhuku zodwala kapena zophedwa kuchokera malo ena kupita dela lina
  • Matenda a Gumburo amatha kupha theka la khola lonse la nkhuku.

Zizindikiro za Gumboro

  • Kusasangalala
  • Kusadya
  • Kumwa madzi ambiri mowilikiza
  • Nkhuku yodwala imakhala chonyonyomala
  • Nkhuku imatsegula mmimba mwa zitosi zobiriwira
  • Mapiko amalendewera ndipo m’nthenga zimanyankhalala
  • Nkhuku zodwala zimatha kufa masiku ochepa chidwalirireni.

Kuteteza

  • Onetsetsani kuti m’khola ndi mwa ukhondo nthawi zonse
  • Sesani mkhola ndi kutsukiramo makhwala opha tizirombo otchedwa formalin wa 4%
  • Osalowetsanso nkhuku zina mkholamo mpaka patatha sabata imodzi
  • Nkhuku zosiyana misinkhu zisawetedwe pamodzi
  • Pewani kukayendera makola a anzanu
  • Perekani katemera ku nkhuku zanu ndi katemera wotchedwa Bursin-2 pamene nkhuku zamaliza sabata imodzi, bwerezani pamene zamaliza sabata zitatu
  • Onetsetsani kuti nkhuku zonse zodwala zachotsedwa pakati pa zina

Kamwazi wa Nkhuku

  • Matendawa amagwira nkhuku zamtundu uli wonse komanso msinkhu uli onse
  • Matendawa amayambitsidwa ndi tizirombo ta mtundu wa Coccidia
  • Tiziromboti timagwira ndi kuswana m’matumbo a nkhuku
  • Matendawa amafala kudzera muchakudya, madzi, utuchi, ziwiya, anthu kapena ziweto zina zomwe zagwedwa zitosi zokhala ndi mazira a tiziromboti.
  • Tizirombo timeneti tikhoza kukhala ndi moyo mu utuchi kapena mudothi kwa chaka

Zizindikiro za Kamwazi

  • Kusasangalala
  • Mapiko amalendewera ndipo nthenga zimanyankhalala
  • Zitosi zosakanikira ndi magazi kapena za madzimadzi

Kupewa matenda a Kamwazi

  • Onetsetsani kuti mukuchita ukhondo mu khola
  • M’khola mudzikhala mouma nthawi zonse
  • Nkhuku zisathinane m’khola ndipo onetsetsani kuti mukusunga nkhuku zofanana misinkhu mkhola limodzi
  • Perekani mankhwala otchedwa Triple Sulpher, ESB3 kapena Amprolium kwa nkhuku zimene zikusonyeza zizindikiro za matendawa
  • Patulani nkhuku zodwala ndi kuzisunga pazokha.

Nthomba

  • Matendawa amagwira nkhuku za msinkhu uli wonse
  • Tizirombo tamtundu wa vayilasi ndito timayambitsa
  • Tiziromboti timalowa mthupi la nkhuku kudzera muzironda za mkamwa, pa lipombo ndi pa gawo liri lonse la thupi
  • Tiziromboti timapilira ku nyengo zouma moti titha kukhala mpaka zaka 10 munyengozi
  • Matendawa amafala mwa pang’ono pang’ono ndipo atha kukhalabe mkhola mpaka miyezi itatu

Zizindikiro za Nthomba

  • Amayamba ndi timatuza toyera tomwe kenako timauma nkuoneka tabulawuni pa lipombo ndi kunkhope ya nkhuku
  • Pakutha pa sabata ziwiri kapena zitatu timauma
  • Matendawa akakhodzokera, zizindikiro zimaoneka m’miyendo ndi mthupi lonse. Matuzawa akasupulidwa amaoneka ngati chilonda cha tsopano
  • Matendawa amapha nkhuku koma osati kwambiri, komabe nkhuku zoyikira zimaikira mochepera

Kuteteza

Perekani katemera wotchedwa poxine pakati pa masabata 7 mkapa 16 akubadwa. Katemerayu amabayidwa mu phiko. Ndipo popereka katemera uzani alangizi akuthandizeni.

Chimfine

  • Matendawa amayambitsidwa ndi tizirombo ta mtundu wa bakiteria
  • Nthawi zambiri amatendawa amabwera mwa mphamvu kwambiri nthawi zinanso amatha kukhala nthawi yayitali m’nkhuku asanathe, koma amafala kwambiri
  • m
  • Amatupitsa gawo la kumutu ndi mphuno za nkhuku
  • Tizirombo toyambitsa matendawa timalowa mthupi la nkhuku kudzera mmaso ndi mu mphuno.
  • Tiziromboti timatha kukhala kunja kwa thupi la nkhuku kwa masiku awiri kapena atatu komabe sitichedwa kufa ndi kutentha.

Matendawa mungawazindikire powona izi ku nkhuku:

  • Kutupa maso ndi kholingo
  • kuvutika kupuma
  • Kutuluka mamina onunkha
  • kusiya kuikira mazira ndi
  • kuyetsemula.

Choyenera kuchita tikaona chimodzi mwa zizindilirozi

  • Matendawa ndi ochizika
  • Kaguleni mankhwala oyenera monga Streptomycin, Dihydrostreptomycin polumikizana ndi alangizi aziweto.

Nthata za Nkhuku

Iti nditizirombo tomwe timayamwa magazi mthupi la nkhuku

Zizindikiro

  • Tiziromboti timaoneka pa thupi la nkhuku
  • Nkhuku zimaoneka zosowa mtendere
  • Zimadzikandakanda
  • Pena zimakonda kusamba mfumbi, mchenga, utuchi kapena phulusa
  • Nkhuku zimaoneka zoperewera magazi mthupi ndipo lioombo limaoneka lotuwa ndi lofota

 

Kuteteza kwake

  • Sesani mkhola tsiku ndi tsiku
  • Kwa nkhuku zomwe ziri ndi nthata zithireni mankhwala otchedwa Actelic pauda ndi kuwazanso mkhola.

Njoka za m’mimba

  • Nkhuku nazonso zimadwala njoka za mmimba
  • Nkhuku zimagwidwa ndi njoka za m’mimba kudzera mu zakudya ndi madzi omwe agwera zitosi zokhala ndi mazira a njoka za m’mimba.

Zizindikiro za Njoka za m’mimba

  • Nkhuku zimachepa magazi, zimanyentchera ndipo zimapinimbira (sizikula bwino)
  • Nkhuku zoikira mazira zimasiya kuikira
  • Nkhuku zimatsegula m’mimba

Zoyenera kuchita tikaona zizindikirozi

  • Tizipatse mankhwala nkhuku zathu zikafika masabata 17 kenako pakapita masiku 21 kenakonso pakatha miyezi itatu iri yonse
  • Kaguleni mankhwala a njoka za m’mimba kumasitolo kapena kafunseni kwa a langizi a ziweto

Kuteteza nkhuku ku Njoka za m’mimba

  • Tsatirani ukhondo wa mkhola
  • Perekani mankhwala opha njoka za m’mimba monga Piparazine nthawi ndi nthawi monga kumayambiliro a nyengo ya mvula ndi ku mathero a nyengo ya mvula

 Tsatirani ndondomeko ya katemera kuti nkhuku zanu zitetezedwe motere:

 Katemera wa nkhuku za mazira:

 Katemera wa nkhuku za nyama:

Share this Doc