NKHUKU ZA MAKOLO
NKHUKU ZA MAKOLO
Kusankha nkhuku zoweta
- Sankhani nkhuku zimene zimakula msanga, zazikuluzikulu, zoswa kwambiri komanso zolera bwino anapiye
Kukwatitsa nkhuku za makolo ndi za Mikolongwe
- Kwatitsani nkhuku za makolo ndi tambala wa Mikologwe kuti zikhale zokula mwamsanga, zoyikira mazira ambiri ndi kupereka nyama yochuluka
- Tambala mmodzi mpatseni nkhuku zazikazi khumi (10)
Kusankha mazira oyenera kufungatira
- Sungani mazira pamalo ouma, aukhondo, opanda fungo lina liri lonse kuti mazira asaonongeke
- Onetsetsani kuti mazira oyenera kufungatira asapitilire masiku 10 kuchokera tsiku limene nkhuku zayikira
- Sankhani mazira opanda chilema
- Sakhani mazira akuluakulu
- Lembani tsiku lomwe dzira laikiridwa padzira kuti mudziwe lomwe lakhalitsa
- Chotsani mazira amene akhala nthawi yaitali, kuti nkhuku ikhalire okhawo amene sanapitirire masiku khumi (10) ataikiridwa