ZAKUDYA NDI KADYETSEDWE KA NKHUKU
ZAKUDYA NDI KADYETSEDWE KA NKHUKU
- Nkhuku zamakolo zimadzipezera chakudya zokha tikatsegulira
- Zipatseni zakudya zowonjezera m’mawa ndi madzulo monga madeya, chimanga, zakudya zotsalira kukhitchini, ndiwo za masamba, ndi zakudya zopanga nokha kuti nkhuku zikule mwa thanzi.
- Zidyetseni zikhokhombe za mazira zopera kuti zidzaikire mazira azikhokhombe zolimba.
- Pangani chakudya cha nkhuku nokha posakaniza zinthu izi:
- Magawo awiri a mgaiwa kapena madeya a chimanga
- Gawo limodzi la ufa wa soya wokazinga ndi
- kamchere pang’ono.
- Sungani anapiye m’khola (basket layering) kuti azipatsidwa chakudya chokwanira ndichoyenera, komanso kuti anapiye akule bwino ndi kutetezeka kuzirombo monga a khwangwala ndi mbalame zina.
- Zipatseni madzi abwino nkhuku nthawi zonse
Chomwera madzi
- Kuti mudziwe zambiri za zakudya ndi kadyetsedwe ka nkhuku kafunseni kwa alangiza a ziweto m’dera lanu
Kuti nkhuku zanu zikhale ndi thanzi tsatirani izi:
- Samalirani ndi kudyetsera bwino nkhuku zanu
- Zipatseni katemera wa Lasota pa miyezi itatu ili yonse kapena I2 pa miyezi inayi iliyonse kuti muteteze nkhuku kumatenda a chitopa
- Musapereke katemera kunkhuku zomwe zikudwala
- Zimwetseni nkhuku mankhwala wopha njoka za m’mimba makamaka miyezi yapakati pa Disembala ndi Malichi pamene mvula ikugwa kuti nkhuku zikule ndi thanzi
- Tenthani kapena kwilirani nkhuku zonse zimene zafa ndi matenda kuopetsa kufala kwa matendawo.