KUSOSA NDIKUKONZEKERA MUNDA WA MPUNGA
KUSOSA NDIKUKONZEKERA MUNDA WA MPUNGA
- Sosani malo amene mulimepo mpunga nthawi yabwino
- Gaulani mukangokolola nthaka idakali ndi chinyontho chokwanira
- Gaulani munda wanu kuti zinyasi ziwolerane bwino kunthandizira kupanga manyowa kuti mizu ya mbewu idzamere bwino ndikupita pansi komanso kuti mphweya wamnthaka uzizayenda bwino mukatero phwanyani mabuma/ziguluma ndikusalaza
- Zinyalala komanso zotsalira zambewu mukakolola zisaotchedwe mcholinga chofuna kusunga michere yofunikira munthaka yochoka kuzotsalirazi komanso kukana kuonjezera mphweya oyipa owononga chilengedwe umwe umachoka kuzootchazi kupita mlengalenga.
- Gawani munda wanu muma poloti otalika 10 mitala ndi 10 mitala mulifupi kenaka kukonza migura m’mbali yodekhetsera madzi.