ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

KUTETEZA MPUNGA KU TIZILOMBO

KUTETEZA MPUNGA KU TIZILOMBO

Pali njira zosiyanasiyana zovomelezeka posamalachilengedwe pamene tikuthana nditizilombo tomwe timaononga mbewu ya mpunga monga; kudzala mbewu zopirira kutizilombo, kudzala mbewu yovomekezeka, kutsatila ndondomeko zakalimidwe ndizina zambiri. Mankhwala ophera tizilombo amagwiritsidwa ntchito ngati kuononga kwa tizilomboti kwadutsa muyeso.

Mbalame

  • Mbalame ndi tizilombo tomwe timaononga kwambiri mpunga ndipo tili ndi kuthekera kwakukulu kochepetsa zokolola ndi gawo lalikulu
  • Mbalame zikuyenera kumaopsyezedwa kuti zichoke m’munda
  • Mpheta/Dzanjo (Quelea quelea) ndi Tchete (Weaver bird) ndi mwa mbalame zovuta kwambili zomwe zimaononga mpunga.

 

Weaver bird (Ntchete)

Ziwala za Bwanoni

  • Bwanoni (Ruspolia differens) ndi ziwalazi zowononga kwambiri ndipo ziri ndikuthekera kochepetsa zokolola ndi mulingo wa 80%
  • Zimakonda kudya njere za mpunga zikanali zanthete.
  • Iphani a Bwanoni popopera mankhwala a Fenitrothion 50 EC posungunula 136 mililitazi mu 14 litazi ya madzi ngati muli ndi mpopi waukulu wobelekera kunsana kapena madzi ochuluka 1 lita ngati muli ndi mpopi wa ULV; kapena Carbaryl 85 WP, 85 galamu m’madzi a mulingo wa 14 litazi ngati muli ndi mpopi wobelekera kunsana kapena 1 lita ya madzi ngati muli ndi mpopi wa ULV.
  • Kumbukirani kuti mankhwala ophera tizilombo amagwiritsidwa ntchito pokhatokha ngati kuononga kwa tizilomboti kwadutsa muyeso.

Ntchemberezandonda

 

  • Poperani Carbaryl (Sevin) 85WP pa mulingo wa 85 galamu mu 14 litazi ya madzi mu mpopi woberekera kapena 85 galamu mu 1 lita ya madzi mu mpopi wa ULV.
  • Fenvalerate (Sumicidin) 20EC pa mulingo wa 13 mililitazi mu 14 litazi ya madzi mu mpopi woberekera kapena 13 mililitazi mu 1lita ya madzi mu mpopi wa ULV; Fenitrothion (Sumithion)50EC pa mulingo wa 136 mililitazi mu 14 litaziya madzi mu mpopi woberekera kapena 136 mililitazi mu 1 lita ya madzi mu mpopi wa ULV
  • Muthanso kupopera Steward 150 EC pa mulingo wofanana ndi Carbaryl 85 WP mpunga utamera komanso utafika masabata 9 kapena 10 utawokeredwa
  • Lebaycid (Fenthion) 1 mililita mu 1 lita ya madzi mu mpopi woberekera ngakhalenso ULV
  • Agulugufe enanso akhoza kupoperedwanso nthawi imene mpunga wangomera utadzalidwa mongomera komanso pakatha masabata 3 weeks kapena 6 utawokeredwa.
  • Kumbukirani kuti mankhwala ophera tizilombo amagwiritsidwa ntchito pokhatokha ngati kuononga kwa tizilomboti kwadutsa muyeso.
Share this Doc