KASANKHIDWE KA MBEWU
KASANKHIDWE KA MBEWU
Pali mitundu ingapo ya nandolo yovomerezeka m’Malawi imene mulimi akhoza kusakhapo: yocha nsange, pakatikati komanso mochedwerapo.
Yocha Mwamsanga
- Imacha pakati pa masiku 120 ndi 150
- Imalola madera ambiri m’Malawi muno
- Imafunika kupopera katatu ikayamba maluwa poteteza ku tizilombo.
ICPL 87105
(Source: Guide for Groundnut,Pigeon peas, Sorghum and Finger Millet in Malawi)
- Imalola madera ambiri m’Malawi muno ndipo imacha pa masiku 126 basi
- Imatalika 130 cm
- Ndi yamaso akuluakulu ndipo imabereka matumba 16 a 50 kilogalamu pa ekala
- Sigwidwa ndi chiwawu kawirikawiri chifukwa imacha msanga.
ICPL 93026
(Source-Guide for Groundnut,Pigeon peas, Sorghum and Finger Millet in Malawi)
- Imalola madera ambiri m’Malawi muno ndipo imacha pa masiku 127 basi
- Imakula (137cm) motalikirapo kuyerekeza ndi ICPL87105
- Ndi yamaso akuluakulu ndipo imabereka matumba 16 a 50 Kilogalamu pa ekala.
Yocha Mwapakatikati
Imacha pakati pa masiku 150 ndi 180 ndipo imalola bwino malo okwererako pang`ono.
Mwaiwathu Alimi (ICEAP 00557)
Photo credit -Chitedze
- Mbewu iyi imacha mwapakatikati, pa masiku 159 – 180.
- Yopirira ku matenda a chiwawu ndi matenda ena a munthaka.
- Mbewu yake imakhala ikuluikulu komanso imawoneka yoyererako pang’ono
- Yamaso akuluakulu ndipo imabereka pafupifupi matumba 16 a 50 kilogalamu pa ekala imodzi.
Chitedze 1 (Mthawajuni)
Photo credit –Chitedze RS
- Imacha mwa pakatikati, masiku apakati pa 151 ndi 190
- Imalola madera ambiri m’Malawi muno
- Imachita bwino kwambiri mukayisiya kuti igonere
- Imapilira ku matenda ena koma imatha kugwidwa ndi matenda a chiwawu
- Imabereka pakati pa matumba 20-24 a 50 kilogalamu pa ekala.
- Yofunika kwambiri ku misika yakunja chifukwa simavuta kusenda khungu lake.
Chitedze 2
Photo credit –Chitedze RS
- Imacha mwa pakatikati, masiku pakati pa 151 ndi 190
- Imalola madera ambiri m’Malawi muno
- Imachita bwino kwambiri mukayisiya kuti igonere
- Imapilira ku matenda ena koma imagwidwa ndi matenda a chiwawu
- Mbewu imakhala ikuluikulu ndipo Imabereka pakati pa matumba 20-25 a 50 kilogalamu pa ekala
- Yofunika kwambiri ku misika yakunja.
Yocha mochedwa
Sauma (ICPL 9145 )
(Source-Guide for Groundnut,Pigeon peas, Sorghum and Finger Millet in Malawi)
- Iyi ndi mbewu yocha mochedwa pakati pa masiku 220 ndi 270
- Yopirira ku matenda a chiwawu ndi nthomba
- Mbewu iyi imakhala ndi maso akuluakulu komanso imabereka pafupifupi matumba 20 olemera 50 kilogalamu pa ekala ngati yalimidwa payokha
- Mbewu iyi imachitanso bwino ngakhale kuibzala ndi mbewu zina.
Kachangu (ICEAP0040)
(Source-Guide for Groundnut,Pigeon peas, Sorghum and Finger Millet in Malawi)
- Mbewu iyi imacha mochedwerako pakati pa masiku 190 ndi 240.
- Yopirira ku matenda a chiwawu
- Yamaso akuluakulu, yobereka kufika matumba 14 a 50 kilogalamu pa ekala ngati yalimidwa payokha.
- Imachitanso bwino kuibzala mophatikiza ndi mbewu zina.