KUTHIRA FETEREZA
KUTHIRA FETEREZA
Kuti mukolole zambiri kumafika makiloglamu 1200 mpaka 1600 pa ekala, thirani inokulanti ndi fetereza wa 23:10:5+6S+1.0Zn wochuluka makilogalamu 80 pa ekala. Tengani fetereza wodzadza makapu nambala 5 awiri kapena tidzitsekerero tiwiri ta Fanta ndi kuthira pa mkwasa wotalika mita imodzi (1m). Thirani fetereza mukangobzala kumene kapena mbewu zikangotuluka kumene.