ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

KUPALIRA

KUPALIRA

Mungathe kuchotsa udzu ndi manja kapena mankhwala.

Kuchotsa udzu ndi manja

Zulirani kapena chotsani udzu m’munda pakangotha sabata imodzi kenaka pamene mwaona kuti udzu wameramo m’munda mwanu. Pewani kuzulira kapena kuchotsa udzu mvula ikangogwa koma pamene kuli dzuwa chifukwa izi zimathandiza kumeretsanso udzuwu.

Kuchotsa udzu ndi mankhwala

Pali mitundu iwiri ya mankhwala yomwe imagwiritsidwa ntchito, okupha njere komanso okupha udzu ukamera monga awa; round up, harness, dual magnum ndi ena ambiri.

Tsatirani malangizo omwe amalembedwa mukamagwiritsa ntchito mankhwalawa. Gulani mankhwala ku malo ovomerezeka!!!!

Valani modziteteza pa nthawi yomwe mukuthira mankhwala.

Farmer in protective wear

Kugwiritsa ntchito njira zamakolo

Chitani ulimi wakasakaniza, kubzala moyenerera, kugalauza, kudyetsera ng’ombe ndi njira zina zochepetsera kuchulukana kwa udzu m’munda.

Share this Doc