ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

KUPALIRA

KUPALIRA

Palirani munda wanu mwachangu udzu ukangomera, chifukwa udzu umalimbirana ndi mbewu yanu chakudya chamthaka komanso madzi.

Tetezani chimanga ku udzu pogwiritsa ntchito njira yongozula kapena mankhwala, kapena kuphatikiza njira zonse. Palirani udzu kosachepera kawiri pamasabata asanu ndi imodzi (6) chimanga chikangomera.

 Kugwiritsa ntchito makasu ndi manja

Palirani kapena zulirani udzu koyamba masabata awiri asanathe, ndipo kupalira kwachiwiri kuchitike masabata asanu ndi imodzi (6) asanathe kapena pamene mwaona kuti udzu wamera.

Phimbirani nthaka ndi mapesi kapena udzu omwe ulibe njere, chifukwa udzu wanjere umafesa njere zake zomwe zimachulukitsa vuto la udzu m’chaka chotsatira.

Palirani pamene kuli dzuwa ndipo pewani kupalira pamene mvula ikugwa chifukwa udzu siumafa.

Njira zina zochepetsera udzu ndi izi: Kasinthasintha wa mbeu, . Onetsetsani kuti mmunda wanu mulibe udzu nthawi zonse.

 

Kugwiritsa ntchito mankhwala

Pali mitundu iwiri ya mankhwala yomwe imagwiritsidwa ntchito kupha udzu; Pali mankhwala opha njere komanso pali mankhwala opha udzu ukamera. Afunseni alangizi za mankhwala oyenera kuthira ndi kathiridwe kake. Mankhwala opha njere kapena udzu athiridwe dothi likadali ndichinyontho.

Welengani bwino ndikutsatira malangizo akagwiritsidwe ntchito kamankhwalawa amene alembedwa pabotolo.

Gulani mankhwala ku malo ovomerezeka!!!!

Share this Doc