MATENDA
MATENDA
Dzimbiri (Gray leaf spot)
Zotsatila
- Chimagwira masamba am’munsi kupita m’mwamba.
- Chimanga chimaoneka chowauka
Kuteteza Kwake
- Kutsatira njira zakalimidwe kabwino.
- Kukonza mmunda msanga kuti zotsalira zam’munda ziwolerane tisanadzale.
- Kasinthasintha wa mbeu
- Kuzula ndi kutentha mbeu zonse zogwidwa ndi matenda.
- Kubzala mbeu zopirira ku Dzimbiri.
Kuwora kwa mizu (Root Rot)
Zotsatila
Zimagwira mizu kupangisa kugwa kwa chimanga
Kuteteza Kwake
- Mbeu yopirira kumatendawa
- Gwiritsani mbeu yovomelezeka
Kuwora kwa Chisononkho (Cob rot)
Zotsatila
Matendawa amagwira ku chitsononkho
Kuteteza Kwake
- Bzalani mbeu yopilira kumatendawa
- Kololani msanga
- Wumitsani bwino chimanga musanasunge.
Namzikambe (Downy mildew)
Zotsatila
- Kukula mokwinimbira
- Kusabereka
- Masamba amapanga chikasu komanso mizere
Kuteteza Kwake
- Kuzula ndi kutentha mbeu zonse zagwidwa ndi nthendayi.
- Kasintha sintha wa mbeu.
- Kubzala moyambirira
- Kugwiritsa ntchito mbeu zovomerezeka
Dzimbiri (Rust)
Zotsatila
Limagwira pena pali ponse pa chimanga
Kuteteza Kwake
- Kudzala mbeu yopilira
- Kasakaniza wa mbeu
Chiwawu (Leaf Blight)
Zotsatila
Chimagwira chimanga chaching’ono
Kuteteza Kwake
- Gwiritsani mbeu yovomelezeka
- Thirani mankhwala a fungicides.
Kontho (Smut)
Zotsatila
- Kunyentchera
- Kukwinimbira kwa masamba
- Kumera kwa masamba paliponse
Kuteteza Kwake
- Gwiritsani mbeu yoti iri ndimankhwala
- Kusamalira mbeu m’munda (Ukhondo m’munda)
- Kugwiritsa ntchito mbeu yovomelezeka
Funsani alangizi azaulimi kapena agro-dealer za momwe mungathirire mankhwala oyenerera komanso moyenerera.