MATENDA
MATENDA
Matenda a mtedza ndi Khate la mtedza kapena kuti kandukutu (rosette), Nthomba yoyambirira, Nthomba yochedwerapo, Dzimbiri ndi Chuku.
Khate la mtedza kapena kuti kandukutu (rosette)
-
Matendawa amayamba ndi kachilombo ka virus ndiponso amafala kudzera ku nsabwe ndi mbozi zoyera
-
Matendawa amatha kuwonongeratu munda wonse wa mtedza
Kuteteza
-
Bzalani moyambirira
-
Palirani m’munda
-
Chotsani ndi kuwotcha mbewu zonse za matenda
-
Bzalani mbewu zopilira ku kandukutu pobzala mbewu monga Chalimbana, Nsinjiro, Chitala ndi Baka malo amene muli kandukutu.
Khate / kandukutu /Rosette
Nthomba yoyambirira
Amagwira mtedza ukangomera. Masamba komanso mtengo zimakhala ndi madontho akuda. Matendawa atha kupangitsa kuti mukolore theka la zokolora zanu.
Kuteteza
-
Kufotsera mbewu zonse zamatenda
-
kuthira mankhwala
-
kubzala mwachangu
-
kasinthasintha wa mbewu
-
Kupalira m’munda
Nthomba yoyambirira
Nthomba yochedwerapo
Masamba amakhala ndi madontho akuda akulu. Matendawa atha kuchepetsa zokolola koposa theka.
Kuteteza
-
kufotsera mbewu zonse zogwidwa ndi matenda
-
kasinthasintha wa mbewu
-
Kupalira m’munda
Nthomba yochedwerapo
Dzimbiri
Kunsi kwa masamba kumakhala madontho a chikasu.
Kuteteza
-
M’munda mukhale mwaukhondo
-
kufotsera mbewu zonse zogwidwa ndi matenda
-
kubzala mwachangu
Dzimbiri