KUTHANA NDI CHUKU
KUTHANA NDI CHUKU
Tetezani mtedza ku chuku pochita izi:
-
Bzalani mbewu yabwino komanso yosaonongeka
-
Bzalani mbewu m’mikwasa iwiri pa mzere uliwonse kuti chinyezi chisungike
-
Konzani ngonyeka kapena mabokosi m’munda wa mtedza kuti chinyezi chisungike chomwe chimathandiza kuchepetsa nkhungu yomwe imayambitsa chuku
-
Kumbani mtedza pa nthawi yake ndikuumitsa bwino kuti usachite chuku
-
Wumitsani mtedza pamalo odutsa bwino mphepo komanso osawomba dzuwa lambiri
-
Musawaze madzi posenda mtedza chifukwa madzi amayambitsa chuku
-
Nyamulani mtedza muzipangizo zouma bwino ndi kuusunga pa malo wouma wopanda chinyezi.
-
Tayani kunkhuti kapena kutentha mtedza umene uli ndi nkhungu ndipo musadyetse ziweto.
-
Kuti mudziwe zambiri za kuthana ndi chuku cha mtedza, kafunseni ku Ofesi ya za Malimidwe m’dera lanu.