KUKONZA MUNDA
KUKONZA MUNDA
Konzani munda mvula ikangotha kapena pamene mwamaliza kukolola. Tipulani mozamitsa bwino kuti zotsalira mmunda ziwolerane bwino komanso kuti mpweya udzitha kudutsa bwino.
Mizere
Pokonza mizere, onetsetsani kuti mizere yatalikirana ma sentimita 75 kuchoka pamzere kufika pa mzere wina. Ndipo mizereyo ikhale yokwera ma sentimita 30 kuchoka pansi. Pamalo otsetsereka, konzani mizere mopingasa.