KUTETEZA KU TIZILOMBO NDI MATENDA
KUTETEZA KU TIZILOMBO NDI MATENDA
TIZIROMBO
Mbozi
Zotsatila
Zimadya pomwe chimanga chimamerera
Kuteteza Kwake
1. Kubzala msanga
2. Kuzula chimanga chimene chagwidwa ndi mbozizi
3.Trichlorfon (Dipterex) 2.5 G
4.Endosulfan 35 EC ndi pyrethroids
Tchembere zandonda
Zotsatila
Zimadya masamba
Kuteteza Kwake
Thirani carbarly (Sevin) 85 WP
Mbozi zonga ntchembere zandonda
Zotsatila
Zimadya masamba, mtengo komanso chimanga kuzitsononkho
Kuteteza Kwake
Kasakaniza wa njira zothana ndi zirombo (IPM) Zina mwa njirazi ndi Kulima motsatira malangizo, kupha mbozi ndi manja, kugwiritsa mankhwala a zitsambas (monga Nimu), Kugwiritsa ntchito mankhwala (Steward 150EC, Belt 480SC, Proclaim Fit, Chlorpyrifos 480ec, Deltanex 25EC)
Kanyenyezi/Mphutsi/Matono oyera (White Grabs)
Zotsatila
Amadya mizu ya chimanga
Kuteteza Kwake
- Chotsani ndi manja ndikuzipha
- Thirani chimanga mankhwala a Gaucho musanadzale
- Pangani ulimi wakasinthasintha
- Pakizani chimanga
- Onetsetsani kuti mukugwilitsa ntchito manyowa owolelana bwino
Nankafumbwe
Zotsatila
Amadya chimanga chikasungidwa
Kuteteza Kwake
- Thirani Actelic
- Sungani mmatumba a PICS Bag
Nankafumbwe wamkulu
Zotsatila
Amadya chimanga chikasungidwa
Kuteteza Kwake
- Kololani msanga
- Musasakanize chimanga cha nankafumbwe ndi chabwino
- Malo usungira akhale aukhondo
- Nyikani masaka mmadzi otentha
- Thirani actellic super dust
Makoswe
Zotsatila
Amadya chimanga chikauma
Kuteteza Kwake
1. Kutchera msampha,
2. Kuweta mphaka
3. Mankhwala ovomelezeka
Chiswe
Zotsatila
Chimaononga mapesi zimapangisa kugwa kwa chimanga
Chimadya chimanga chikasungidwa
Kuteteza Kwake
- Mankhwala ovomerezeka ophera chiswe. Tsatirani malangizo akagwiritsidwe ntchito kake amene alembedwa pa botolo lamankhwalawo.
Yenderani munda wanu mopingasa pingasa kuti muone ngati wagwidwa ndi tizilombo kapena matenda.
Ngati mwawona tizirombo kapena matenda pamapesi khumi (10) mwamapesi zana limodzi (100) ali onse omwe mwayendera (10%), poperani mankhwala. Ngati mwawona mbozi zonga ntchemberezandonda pamapesi makumi atatu (30) mwamapesi zana limodzi (100) ali onse omwe mwayendera (30%), poperani mankhwala msanga.
Mankhwala onse ophera tizirombo ali ndi malangizo omwe amalembedwa pa paketi kapena pa botolo omwe amafotokoza za mitundu ya tizirombo tomwe mankhwalawo amapha, muyezo, ndi kagwiritsidwe ntchito kake. Pothira mankhwala valani zodzitetezera.
Tsukani sipuleya katatu, ikani nozolo yopopera tizirombo, valani modziteteza ku mankhwala ndipo poperani chakum’mawa kapena madzulo komanso kulibe mvula.
Dziwitsani alangizi azaulimi ngati mwaona kuti munda wanu wagwidwa ndi tizirombo toononga.
Sungani mankhwala patali ndi ana chifukwa ndi oopsa.