ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

MATENDA

MATENDA

Dzimbiri (Gray leaf spot)

 Zotsatila

  • Chimagwira masamba am’munsi kupita m’mwamba.
  • Chimanga chimaoneka chowauka

Kuteteza Kwake

  • Kutsatira njira zakalimidwe kabwino.
  • Kukonza mmunda msanga kuti zotsalira zam’munda ziwolerane tisanadzale.
  • Kasinthasintha wa mbeu
  •  Kuzula ndi kutentha mbeu zonse zogwidwa ndi matenda.
  • Kubzala mbeu zopirira ku Dzimbiri.

Kuwora kwa mizu (Root Rot)

 Zotsatila

Zimagwira mizu kupangisa kugwa kwa chimanga

Kuteteza Kwake

  • Mbeu yopirira kumatendawa
  • Gwiritsani mbeu yovomelezeka

Kuwora kwa Chisononkho (Cob rot)

 Zotsatila

Matendawa amagwira ku chitsononkho

Kuteteza Kwake

  • Bzalani mbeu yopilira kumatendawa
  • Kololani msanga
  • Wumitsani bwino chimanga musanasunge.

Namzikambe (Downy mildew)

 Zotsatila

  • Kukula mokwinimbira
  • Kusabereka
  • Masamba amapanga chikasu komanso mizere

Kuteteza Kwake

  • Kuzula ndi kutentha mbeu zonse zagwidwa ndi nthendayi.
  • Kasintha sintha wa mbeu.
  • Kubzala moyambirira
  • Kugwiritsa ntchito mbeu zovomerezeka

Dzimbiri (Rust)

 Zotsatila

Limagwira pena pali ponse pa chimanga

Kuteteza Kwake

  • Kudzala mbeu yopilira
  • Kasakaniza wa mbeu

Chiwawu (Leaf Blight)

Zotsatila

Chimagwira chimanga chaching’ono

Kuteteza Kwake

  • Gwiritsani mbeu yovomelezeka
  • Thirani mankhwala a fungicides.

Kontho (Smut)

 Zotsatila

  • Kunyentchera
  • Kukwinimbira kwa masamba
  •  Kumera kwa masamba paliponse

Kuteteza Kwake

  • Gwiritsani mbeu yoti iri ndimankhwala
  • Kusamalira mbeu m’munda (Ukhondo m’munda)
  • Kugwiritsa ntchito mbeu yovomelezeka

Funsani alangizi azaulimi kapena agro-dealer za momwe mungathirire mankhwala oyenerera komanso moyenerera.

Share this Doc