ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

DONGOSOLO LA MADZI

DONGOSOLO LA MADZI

  • Kukhazikitsa dongosolo labwino la kasungidwe ndi kagwiritsidwe ntchito kabwino ka madzi pa munda ndi chinthu chofunikira kwambiri. Izi ndi zinthu monga kukonza migula yoti isunge madzi, kukumba ngalande zodutsamo madzi komanso kuika malo olowera ndikutulukira madzi. Izi zimathandiza kuti pa munda pakhale madzi okwanira nthawi yonse yaulimi
  • Dongosololi limasiyana pa munda wa nthirira ndi wa mvula
  • Onetsetsani kuti muli ndi madzi okwanira kuyambira nthawi mwadzala/kuwokera mpunga kufikira kukhwima
  • Lolani madzi akhale mmunda wa mpunga ozama 5 sentimita koma osadutsira 10 sentimita kufikira mpunga utakhwima kuti mphamvu ya mchere wa Nitrogen usatuluke
  • Mukalima mpunga munjira ya SRI, thirirani pokhapokha thaka ya mmunda wanu wa mpunga itauma ndi kuyamba kung’ambika pang’ono koma mbewu zisanafote kwambiri (onani chithunzi pansipo). Madzi asakhale mmunda kwa nthawi yaitali.

  1. Flooded 5-10cm B. Intermittent period C. Hairline cracks

Field showing hairline cracks ©S, Hidayah et al.

Share this Doc