KAKONZEDWE NDI KUFESEDWE KA MPUNGA PA NAZALE
KAKONZEDWE NDI KUFESEDWE KA MPUNGA PA NAZALE
- Pali mitundu iwiri ya kapangidwe ka manazale ampunga; Nazale ya pamtunda (dry seed bed) komanso nazale ya mkati mwa munda (wet seedbed)
- Konzani nazale moyambirira kuti nthawi yofesa ndikuokera ikhaleso mu nthawi yake.
Nazale ya mkati mwa munda wa mpunga (Wet seed bed)
- Nazale imeneyi imakonzedwa mkati mwa munda umene mbande za mpunga zimadzawokeredwamo panthawi imene madzi afika pamlingo wabwino wowokekera
- Nazaleyi imakonzedwa mofanana ndi magawo a munda am’mene mukukonzera kuzawowokeramo mpunga ukafika pamlingo wowokera
- Madzi othirira nazale ndi madzi omwe akuyenda okha m’munda wa mpunga.
Nazale yaku mtunda (Dry seed bed)
- Nazale imeneyi imapangidwa kunja kwa munda wa mpunga, mchitidwemu umachulukira kumadera amene amalima mpunga wakumitunda
- Imagwiritsidwa ngati mukulima mpunga wakucha mwapakatikati ngati Faya14M69 ndi Kilombero umene ukhoza kukhala pa nazale masiku 28 kufikira 35 days osaonongeka pokawokera mvula ikayamba
- Konzani nazale m’mbali mwa munda umene mudzadzale mpunga wanu pafupi ndi madzi othiririra komanso pakhale pamalo oti sungamizidwe ndi madzi ngati mvula yabwera.
Kufesa mbewu pa nazale
- Mbewu yochuluka 63 kilogalamu ya lokolo ndiyokwanira malo okwanira maekela awiri ndi theka pamene mbewu yamakono pafunika 75 kilogalamu pa hekitala.
- Ngati mukulima mpunga m’njira ya umodziumodzi, System of Rice Intensification (SRI), 12 kilogalamu ya mbewu ndi yokwanira malo okwanira maekela awiri ndi theka
- Fesani mbewu pa mabedi athyathyathya otalika 20mita ndi 1mita mulifupi okwera 5 sentimita m’mwamba
- Mabedi 20 ngati amenewo amakwanira kukhala ndi mbande zokwanira maekela awiri ndi theka
- Ngati mukulima mpunga munjira ya SRI, mabedi 20 otalika 5 mita nd 1mita mulifupi ndiokwanira maekela awiri ndi theka
- Pa mwamba pa bedi la nazale ikanipo saka la feteleza
- Pa mwamba pa masaka a feteleza ikanipo dothi lochokera m’munda umene mudzale mpunga losakaniza ndi manyowa owolerana bwino
- Mwazani mbewu mofanana pa bedi lonse koma mosathithikana kuchepetsa kupikisana pa chakudya komanso malo
- Wazanipo manyowa kapena dothi lomasuka kapenanso mchenga
- Ngati nthaka ya nazale siyachonde, thirani 500 galamu ya feteleza wa 23 :21 :0+4S pa bedi lotalika 5 mita ndi 1mita muli fupi
- Phimbirani nazale yanu kusunga madzi komanso kuteteza mbewu yanu ku dzuwa
- Thirirani nazale zanu ngati zikuonetsa kufota nthawi ya m’mawa, masana ndi madzulo
- Nazale zanu zisakhale ndi madzi amene akhazikika ngati m’munda mwa mpunga
- Chotsani udzu pa nazale zanu ukanali wa ung’ono ung’ono pafupipafupi.