KATHILIDWE KA FETELEZA
KATHILIDWE KA FETELEZA
- Feteleza wa 23:10:5+6S+1.0Zn ndi UREA ndiamene ali ovomerezeka ku Malawi kuno pofuna kuwonjezera mchere wa Nitrogen mu nthaka
- Pa SRI nkhani ndiya manyowa ndi feteleza ochepa. Thirani 16000 kilogalamu ya manyowa ndi 12kilogalamu ya 23:10:5+6S+1.0Zn ndi 43 kilogalamu ya Urea pa hekitala.
Mpunga wa Faya 14M-69 komanso mitundu ina
- Faya 14-M-69, Kilombero komanso mitundu ina ya mpunga imafunika mchere wa nitrogen wokwanira 60 kg komanso wa Phosphate wochuluka 25kg pa maekala awiri ndi theka
- Izi zingatheke pamene mlimi wathira feteleza wokwanira 100 kilogalamu wa 23:10:5+6S+ 1.0Zn patangotha masiku 20 kuchokera pomwe mbewu yamera komanso 50 kilogalamu wa Urea patangotha masiku 60 mbewu itaphukira.
Mpunga wa Senga (IET 4094) komanso mitundu ina
- Mpunga wa Senga (IET 4094), Changu (IR 1561- 250-2-2), Nunkile (Pusa 33), Mtupatupa (Taichung Sen 10) komanso wa Vyawo (ITA 302), umafuna 80 kilogalamu ya mchere wa nitorojeni komanso 25 kilogalmu ya Fosifolasi (P2O5) pa maekala awiri ndi theka
- Kuti mukwanitse kuchuluka kwa milingo imeneyi mukuyenera kuthira feteleza wa 23:10:5+6S+ 1.0Zn wokwanira 100 kilogalamu komanso wa Urea wokwanira 5 kilogalamu payekha panthawi imene mukuwokera mpunga
- Feteleza aliyense akuyenera kuthiridwa payekha pofuna kuti malo onse alandire mulingo wofanana
- Pakatha masiku 40 kuchokera pamene mwawokera mpunga thirani Urea wokwanira 100 kilogalamu pa maekala awiri ndi theka. Chitani izi kwa mbewu zina zonse za mpunga kupatula wa Nunkile umene mukuyenera kuwuthira feteleza wongowaza patangotha masiku 25 kuchokera pomwe mpunga wamera.