KUBZALA
KUBZALA
Mpunga ukhoza kubzalidwa m’mapando mvula isanabwere kapena ndi mvula yoyamba komanso kuokeredwa mbande kuchokera pa nazale.
Kudzala m’mapando kapena kuwaza (Dibbling or Broadcasting)
- Mpunga ukhoza kubzalidwa mmunda mvula isanabwere kapena ndi mvula yoyamba
- Dzalani njere za mpunga 6 pa mapando otalikirana 23 sentimita komanso 23 sentimita muli fupi
- Patulirani kapena pakizani mpunga wanu patatha masiku 15 kapena 20 kuti ukhalepo 4 pa phando limodzi.
Kudzala mpunga njira yowokera
Mpunga ukhoza kuokeredwa munjira yakale kapena ya umodziumodzi (SRI)
Njira yakale yamakolo yowokera mpunga
- Okerani mbande za masiku 15 kulekeza 25 mu nthawi ya mvula komanso za masiku 20 kulekeza 30 mu nthawi ya mwavu
- Okerani mbande 3 kapena 4 pa phando lililose lotalika 23 sentimita mulitali ndi 15 sentimita muli fupi kufikira paphando lina.
Kuwokera mpunga kudzera mu njira ya umodzi umodzi (SRI, System of Rice Intensification)
- SRI ndi njira yolimira mpunga yomwe imathandiza kuchulutsa zokolola pochepetsa mavuto monga; kagwiritsidwe ntchito ka madzi kosalongosoka, kuchepekera kwa chonde mu nthaka ndi kuchepetsa udzu potsata kalimidwe koyenerera
- SRI imathandiza kuchulutsa zokolola pa malo kudzera ku kagwiritsidwe ntchito kabwino ka madzi komanso kuchepetsa ndalama zotuluka kudzera mukulipira antchito komanso kugula zipangizo
- Njirayi imakhala bwino kwambiri pa ulimi wa nthirira koma imagwiraso pa ulimi wa mvula
SRI imatha kuchulutsa zokolola kuchoka pa 2 tani pa maekala awiri ndi theka kufika pa 7 tani. (Pa tani iliyonse pa makhala mathumba 20 a 50kg).
Nsanamila za SRI (System of Rice Intensification)
SRI ili ndi nsanamira/ndondomeko 6 zomwe zimatsatiridwa monga:
- Kuwokera mbande za mpunga zikakwanitsa masiku khumi kuchokera pa tsiku lomwe zinamera
- Kuwokera mbande imodzi pa phando limodzi
- Kuwokera mbande m’magawo ofanana mulitali komanso mulifupi pa mulingo wa 23 sentimita
- Kuthira manyowa okwana 1600 kilogalamu pa poloti imodzi ya theka la theka la ekala (0.1ha), Feteleza okwana 12 kg 23:10:5+6S+1.0Zn ndi 4.3 kg urea pa ndime yokwana 0.1ha
- Kuonetsetsa kuti muzitsekula ndikutseka madzi kuti mbande zizikhala ndimpata omizidwa komanso okhala pa mtunda. Zisakhale mmadzi nthawi zonse
- Kugwiritsa ntchito chipangizo cha cono weeder pofuna kuthana ndi udzu.