KUKOLOLA NDI KUSAMALIRA MPUNGA
KUKOLOLA NDI KUSAMALIRA MPUNGA
- Kololani pamene mpunga wanu wakhwima ndi kuuma ndipo wayamba kuwonetsa mtundu wokhala ngati golide. Onetsetsani kuti izi zikuwoneka pafupifupi magawo atatu mwa anayi (¾) a m’munda mwanu
- Kololani mpunga pakatha masiku a pakati pa 8 ndi 12 kuchokera pamene wakhwima munthawi ya dzinja komanso pakati pa masiku 4 ndi 8 munthawi ya chirimwe kuti mukolole mpunga wabwino wosasweka (mapesi ake akhale akanali awisi)
- Chotsani madzi m’munda wa mpunga kudzera mu ngalande patasala masiku pafupifupi 7 kapena 10 kuti mukolole. Izi zimathandiza kuti uwume mofanana komanso alimi adzayendemo muli mouma.
Kuwomba ndi Kupeta
- Mwetani mpunga ndi chisikiro pa mulingo wa pakati pa 5 ndi 10 sentimita kuchokera pansi ndipo uwombeni tsiku lomwelo
- Izi ndichifukwa chakuti mpunga sumauma mwachangu ukamawumitsidwa pansi uli wosaomba
- Wombani/punthani mpunga wanu pa mkeka kapena pa pepala la pulasitiki la mtundu wakuda pogwiritsa ntchito timitengo ting’ono ting’ono kapena timitolo ta mpunga womwewo
- Petani kapena wuluzani mpunga umene waombedwa ndi lichero kuti muchotse zinyalala, mpunga wamphwemphwa/wapepe komanso zinthu zina monga miyala.
Kuwumitsa
- Umitsani mpunga wanu pa dzuwa pa mkeka kwa masiku awiri kuti ufike pa chinyotho mulingo wa 13% chomwe ndichoyenera mukafuna kusunga mpunga wanu kuti usawonongeke
- Mpunga wabwino wosadukaduka umapezeka ngati mwawukonoletsa mutangomaliza kumene kuuwumitsa
- Ngati wasungidwa nthawi yaitali, onetsetsani kuti mwauyanika kaye kwatsiku limodzi musanawukonoletse.
Kusunga
- Sungani pamalo abwino monga m’matumba komanso mu nkhokwe
- Mpunga wosapuntha ukuyenera kusungidwa m’malo opanda chinyontho, opita mphepo komanso otetezeka kutizilombo komanso tinyama towononga monga makoswe
- Mpunga wosapuntha umatha kusungika ngakhale opanda mankhwala koma ngati mukufuna thirani mankhwala aufa a Actellic Super kapena (Bifelthrin) Super Grain Dust pa mlingo wa sachet imodzi yolemera 40-gram pathumba la 50kg la mpunga wosapuntha kuti muteteze ku nankafumbwe wa mpunga.