KUPALIRA UDZU M'MUNDA
KUPALIRA UDZU M’MUNDA
- Gawulani mukangokolola kumene pofuna kuchepetsa kuchuluka kwa tchire m’munda
- Kutipulira m’munda muli madzi ndi njira imodzi yothandiza kuchepetsa udzu m’munda
- Kuzulira udzu ndi manja ndi njira yokhayo yovomerezeka yothana ndi udzu mukadzala mpunga njira yakumwaza nthawi ya mvula
- Muntha kugwiritsa chipangizo cha Cono Weeder popalira munda wa mpunga ngati unadzalidwa mwadongosolo la SRI mumalaini
- Kupha tchire ndi mankhwala kapena kuzulira ndi manja ndizo njira zovomerezeka pa ulimi wa mpunga wa nthirira
- Poperani mankhwala ophera tchire a Ronstar 25 EC pa maekala awiri ndi theka posungunula 3 litazi ya mankhwala m’madzi ochuluka 300 litazi.
- Poperani mankhwalawa pasanathe masiku atatu kuchokera tsiku lowokera mpunga nthaka inakali ndi chinyontho. Ngalande zamadzi zitsekulidwe pakatha masiku atatu.
Dongosolo labwino la madzi likhoza kuthandizanso kuchepetsa udzu chifukwa pali udzu wina umafa ukamizidwa m’madzi.
Kupalira pogwiritsa ntchito cono weeder
Udzu wa Nadanga / Chibakha (Echinochloa crusgalli)
- Nadanga ndi udzu wovuta kwambiri m’munda wa mbewu ya mpunga
- Kumakhala kovuta kusiyanitsa mpunga ndi udzuwu umenewu mpaka nthawi yopanga maluwa kapena yofula
- Kuthana nawo kwake kumakhala kovuta komanso kumachitika mochedwa
- Alimi omwe ali m’madera amene udzu uwu umavuta akuyenera kuphunzitsidwa za momwe angaudziwire udzuwu.
- Alimi akuyeneranso kulangizidwa kuti aziyang’ana udzuwu pafupipafupi kuti awuzulemo
- Kuwokera mpunga m’mizere kumathandiza kuti udzu udziwike mosavuta
- Udzu ukuyenera kuzulidwa ndikutayidwa kutali komwe ukuyenera kukwiriridwa kapena kuwotchedwa
- Ngati pamunda pachuluka udzu wovuta kwambiri, bzalanipo chimanga chaka chinacho kapena mu nyengo ya chilimwe kuti mukwanitse kuzindikira nadanga/chibakha mosavuta komanso ngati njira imodzi yowuchepetsera komanso mutha kusiyapo osalima kwa chaka chimodzi kuti udzuwu ufe.