KUTETEZA MPUNGA KU MATENDA
KUTETEZA MPUNGA KU MATENDA
Mpunga umagwidwa ndi matenda osiyanasiyana koma matenda a Ciwawu ndi Thomba ndi matenda amene ali ovuta ku mpunga ku Malawi kuno.
Chiwawu / Leaf blast
Matendawa amagwira masamba ndipo amaononga mpunga kwambiri.
Zizindikiro zake
- Timadothomadotho ta mtundu wa mtambo wa buluwu pa masamba, timadothoti timakula ndikukhala tozungulira pakati pa khakhi/phulusa ndi mkwaso wozungulira woderadera
- Timadothoti timalumikizana ndipo masamba amaoneka oderadera
- Pa ngalangala ya mpunga pamaoneka timikwaso takuda
- Ngalangala zimafota kenako kufa osabereka mpunga (phwepha).
Kuteteza kwake
Tsatirani ndondomeko za makono zabwino zolimira mpunga ngati izi:
- Tenthani zinyalala zonse zotsalira pokolola mpunga ogwidwa ndi matendawa
- Tenthani zotsalira zonse za mpunga mukakolola
- Palirani ndi kutentha udzu onse mumigula ya madzi komanso ndunda
- Dzalani mpunga motalikirana bwino
- Gwiritsani mbewu ya mpunga yovomekezeka
- Poperani mankhwala ovomekezeka kuti muchepetse matendawa
- Musathire feteleza wochuluka wa mchere wa nitrogen.