KUTETEZA MPUNGA KU TIZILOMBO
KUTETEZA MPUNGA KU TIZILOMBO
Pali njira zosiyanasiyana zovomelezeka posamalachilengedwe pamene tikuthana nditizilombo tomwe timaononga mbewu ya mpunga monga; kudzala mbewu zopirira kutizilombo, kudzala mbewu yovomekezeka, kutsatila ndondomeko zakalimidwe ndizina zambiri. Mankhwala ophera tizilombo amagwiritsidwa ntchito ngati kuononga kwa tizilomboti kwadutsa muyeso.
Mbalame
- Mbalame ndi tizilombo tomwe timaononga kwambiri mpunga ndipo tili ndi kuthekera kwakukulu kochepetsa zokolola ndi gawo lalikulu
- Mbalame zikuyenera kumaopsyezedwa kuti zichoke m’munda
- Mpheta/Dzanjo (Quelea quelea) ndi Tchete (Weaver bird) ndi mwa mbalame zovuta kwambili zomwe zimaononga mpunga.
Weaver bird (Ntchete)
Ziwala za Bwanoni
- Bwanoni (Ruspolia differens) ndi ziwalazi zowononga kwambiri ndipo ziri ndikuthekera kochepetsa zokolola ndi mulingo wa 80%
- Zimakonda kudya njere za mpunga zikanali zanthete.
- Iphani a Bwanoni popopera mankhwala a Fenitrothion 50 EC posungunula 136 mililitazi mu 14 litazi ya madzi ngati muli ndi mpopi waukulu wobelekera kunsana kapena madzi ochuluka 1 lita ngati muli ndi mpopi wa ULV; kapena Carbaryl 85 WP, 85 galamu m’madzi a mulingo wa 14 litazi ngati muli ndi mpopi wobelekera kunsana kapena 1 lita ya madzi ngati muli ndi mpopi wa ULV.
- Kumbukirani kuti mankhwala ophera tizilombo amagwiritsidwa ntchito pokhatokha ngati kuononga kwa tizilomboti kwadutsa muyeso.
Ntchemberezandonda
- Poperani Carbaryl (Sevin) 85WP pa mulingo wa 85 galamu mu 14 litazi ya madzi mu mpopi woberekera kapena 85 galamu mu 1 lita ya madzi mu mpopi wa ULV.
- Fenvalerate (Sumicidin) 20EC pa mulingo wa 13 mililitazi mu 14 litazi ya madzi mu mpopi woberekera kapena 13 mililitazi mu 1lita ya madzi mu mpopi wa ULV; Fenitrothion (Sumithion)50EC pa mulingo wa 136 mililitazi mu 14 litaziya madzi mu mpopi woberekera kapena 136 mililitazi mu 1 lita ya madzi mu mpopi wa ULV
- Muthanso kupopera Steward 150 EC pa mulingo wofanana ndi Carbaryl 85 WP mpunga utamera komanso utafika masabata 9 kapena 10 utawokeredwa
- Lebaycid (Fenthion) 1 mililita mu 1 lita ya madzi mu mpopi woberekera ngakhalenso ULV
- Agulugufe enanso akhoza kupoperedwanso nthawi imene mpunga wangomera utadzalidwa mongomera komanso pakatha masabata 3 weeks kapena 6 utawokeredwa.
- Kumbukirani kuti mankhwala ophera tizilombo amagwiritsidwa ntchito pokhatokha ngati kuononga kwa tizilomboti kwadutsa muyeso.