ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

MITUNDU YA MBEWU YA MPUNGA

MITUNDU YA MBEWU YA MPUNGA

  • Pali mitundu iwiri ya mbewu ya mpunga; mpunga wa lokolo komanso wamakono
  • Alimi amene amagwiritsa ntchito mbewu yamakolo amayenera kusankha mbewu yabwino kenako ndi kuisunga pamalo abwino oti isaonengeke. 

Tebulo yotsatirayi likuwonetsa mitundu yampunga yomwe imalimidwa ku Malawi kuno komanso nthawi yake.

Nyengo yodzalira

Mitundu ya mbewu

Wamthirira

Changu, Senga, Vyawo, Mtupatupa, Nunkile, Kayanjamalo, Mpatsa, Katete, Mpeta and Nazolo

Wamvura

Wambone, Lifuwu, Faya, 14-M-49, Nerica 3, Nerica 4, Kayanjamalo, Mpatsa and Katete

Kum’tunda (mid-high-altitude areas)

Kameme

Mbewu za makono zimachita bwino pakatikati pa ngolo zinayi ndi theka kufikila zisanu ndiziwiri (4.5-7 Mt), pamene mbewu zalokolo zimachita bwino kuyambira ngolo imodzi mpaka zinazi nditheka pa hekitala iliyonse (1 to 4.6 Mt).

Mbewuzi munthawi yaulimi wa mvula zimakhwima makatikati pamasiku 140 ndi 155, pamene munyengo yamthirira ndipakati pamasiku 95 ndi 120.

Share this Doc