ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

MSIKA

MSIKA

  • Mpunga umene mwakonzeka kuti mupititse pamsika ukhale wouma bwino pa mlingo wa wa chinyontho cha 13%, wopanda miyala, zinyalala ndizina zomwe zisali mpunga
  • Ogula akuluakulu a mpunga ndi ADMARC, NASFAM komanso ena amalonda ogula ndikugulitsa
  • Nthawi zambiri ogula amavomera magiredi awiri a mpunga. Giredi loyamba lomwe lilibe mphwemphwa/pepe, lopanda miyala komanso lopanda mpunga wa matenda lomwe amaligula pamtengo wokwera. Wina wonse umagulidwa pa mtengo wa giredi lachiwiri womwe mtengo wake umakhala wotsikirapo
  • Kupatula kugulitsa mpunga wosapuntha, konoletsani mpunga wanu kumalo onse amene anakhazikitsidwa a zaulimi wa mpunga monga ku Domasi, Nkhotakota, Karonga, chigwa cha mtsinje wa Shire komanso Bwanje. Gulitsani kudera kwanu konko pa mtengo woyerekeza ndi momwe kudera kwanuko kuliri. 
Share this Doc