KUBZALA
KUBZALA
Kusankha mbewu
-
Kusankha mbewu yobzala kumatengera kuchuluka kwa zokolola za mbewuyo, kutalika kwa nthawi kuti ikhwime, kupilira kwa mbewuyo ku matenda komanso kudera kumene mukulima
-
Gwiritsani ntchito mbewu yovomerezeka kuchokera ku ma ofesi a zaulimi komanso ma agulodira ovomerezeka
-
Iswani/sendani mbewu ya mtedza nthawi yomwe mukufuna kukadzala
-
Mbewu ya mtedza mutha kuyibwereza kubzala mosapitilira zaka zitatu
-
Afunseni alangizi a boma za mbewu yoyenerera dera lanu.
Kuthira Inokulanti
-
Mungathe kuthira inokulanti ku mbewu yanu ya mtedza kuti ichite bwino
-
Inokulanti mungathe kumugula ku ma ofesi a zakafukufuku a unduna wa za malilidwe komanso kwa ma agulodira ovomerezeka
-
Werengani malangizo akathiridwe ka inokulanti omwe amakhala pa ka paketi ka inokulanti.