KUBZALA
KUBZALA
-
Bzalani mtedza ndi mvula yoyamba pamene mvulayi yagwa yokwanira
-
Kubzala moyambirira kumathandiza kuti mbewuyo ikhwime nthaka ikadali ndi chinyezi
-
Mtedza umachita bwino ngati mbewuyi yabzalidwa pa mulingo woyenera.
-
Lembani /pangani mikwasa iwiri yotalikirani masentimita 20 pa mizere yotalikirana masentimita 75.
-
Bzalani mtedza umodziumodzi motalikirana masentimita 15 pa phando pa mkwasa uliwonse pa mitundu yotambalala, kapena masentimita 10 pa mitundu yoyimilira. Ndipo bzalani mtedza masentimita 5 kapena 6 kulowa pansi. Mutha kubzalanso chonchi pa malo ongosalaza popanda mizere.
Mtedza wotambalala
Mtedza woyimilira
-
Pakizani mbewu ya mtedza mu sabata yoyamba mtedza ukangomera
-
Bzalani makilogalamu 22 kapena 40 pa ekala ngati mukubzala mbewu monga CG7, Nsinjiro ndi Chalimbana
-
Ngati mukubzala mbewu monga Kakoma, chitala, baka, bzalani makilogamu osachepera 20 kapena 24 pa ekala
-
Ndikofunikira kuti masangwe a mtedza adzigwirana kwambiri osaonetsa dothi. Kusiya mipata ndikuonetsa dothi kumaitana nsabwe zomwe zimabweretsa matenda a khate. Mtedza ukagwirana bwino ukadali waung’ono umalepheretsa udzu kumera m’munda.