ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

KUKOLOLA

KUKOLOLA

  • Kukolola mtedza nthawi yabwino kumathandiza kuti mtedza usaonongeke. Pewani kukolola mtedza usanakhwime chifukwa umakhala ndi mafuta ochepa, umakhwinyata komanso sumakhala ndi maonekedwe abwino.

  • Zulani mtedza wochepa kuti muwone ngati wakhwima, ngati mtedza uli ndi madontho akuda (osakhala matenda) mkati mwamakoko ake dziwani kuti wakhwina.

A-matured-groundnut-pod matured gnuts

  • Kugwa kwa masamba sichizindikiro chokwanira kuti mtedza wakhwima.

  • Mukachedwetsa kukolola, mtedza umagwidwa ndi chuku. Ngati masamba a mtedza agwa kwambiri kololanibeni ngakhale usanakhwime kwambiri.

Share this Doc