KUTETEZA KU TIZILOMBO NDI MATENDA
KUTETEZA KU TIZILOMBO NDI MATENDA
Tizilombo
-
Tizilombo tomwe timawononga mtedza kwambiri ndi nsabwe, chiswe, mphutsi zoyera, mbozi ndi Hilda sp
-
Nsabwe ndi zowopsya kwambiri chifukwa zimabweretsa matenda ovuta a khate (otchedwa rosette)
-
Nsabwe zitha kupewedwa pobzala moyambirira komanso pobzala m’mapando moyenerera. Bzalani mitundu ya mbewu ya mtedza yopilira ku khate.
Kuteteza ku tizilombo
-
Chotsani udzu m’munda komanso tchire loyandikana ndi munda wa mtedza
-
Nsabwe zitha kupewedwa pobzala moyambirira, podzala m’mapando moyenerera komanso pochotsa ndi kuwotcha mbewu zonse zomwe zagwidwa ndi matenda
-
Mphutsi zoyera zitha kupewedwa popanga ulimi wakasinthasintha komanso posalima mtedza pa mphanje
-
Mbozi zitha kupewedwa pobzala moyambirira, pobzala m’mapando moyenerera komanso pochotsa ndi kuwotcha mbewu zonse zogwidwa ndi tizilombo kwambiri. Ziwala mutha kuthana nazo pogwira ndi manja kapena kupopera mankhwala ovomerezeka.
-
Tizilombo tovuta kwambiri ta m’dothi ndi monga chiswe, mphutsi zoyera ndi Hilda. Tizilombo tokhala pamwamba pa mtedza ndi monga nsabwe.
Mbozi
Mphutsi zoyera
Nsabwe
Chiwala
Kuti mudziwe zambiri za kuthana ndi tizilombo ta mu mtedza, kafunseni alangizi a za malimidwe m’dera lanu