ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

KUTHANA NDI CHUKU

KUTHANA NDI CHUKU

Aflatoxin

Tetezani mtedza ku chuku pochita izi:

  • Bzalani mbewu yabwino komanso yosaonongeka

  • Bzalani mbewu m’mikwasa iwiri pa mzere uliwonse kuti chinyezi chisungike

  • Konzani ngonyeka kapena mabokosi m’munda wa mtedza kuti chinyezi chisungike chomwe chimathandiza kuchepetsa nkhungu yomwe imayambitsa chuku

  • Kumbani mtedza pa nthawi yake ndikuumitsa bwino kuti usachite chuku

  • Wumitsani mtedza pamalo odutsa bwino mphepo komanso osawomba dzuwa lambiri

  • Musawaze madzi posenda mtedza chifukwa madzi amayambitsa chuku

  • Nyamulani mtedza muzipangizo zouma bwino ndi kuusunga pa malo wouma wopanda chinyezi.

  • Tayani kunkhuti kapena kutentha mtedza umene uli ndi nkhungu ndipo musadyetse ziweto.

  • Kuti mudziwe zambiri za kuthana ndi chuku cha mtedza, kafunseni ku Ofesi ya za Malimidwe m’dera lanu.

Share this Doc