ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

KUWUMITSA NDI KASUNGIDWE

KUWUMITSA NDI KASUNGIDWE

  • Wumitsani bwino mtedza wanu musanawusunge

  • Thotholani mtedza ukauma bwino

  • Mutha kuswa mtedza pogwiritsa ntchito manja kapena makina.

  • Petani mtedza wamakoko ndikuchotsa zinyalala zonse.

  • Sungani mtedza osasenda m’matumba pamalo owuma komanso odutsa mphepo kuti usaonongeke ndi chuku

  • Ngati mukufuna kusunga mtedza wosaswa nthawi yayitali, ikani m’matumba ndikuthira mankhwala a Actellic super dust, funsani alangizi momwe mungathilire mankhwalawa

  • Sanjani matumba a mtedza pa matabwa kapena pa mitengo kuti asakhudze khoma kapena pansi kuopetsa chinyezi

storage- groundnuts

  • Yenderani mtedza wanu pafupipafupi kuti muwone ngati wayamba chuku kapena kuonongeka ndi tizirombo

  • Tetezani mtedza ku makoswe posunga mphaka kapena kutchera misapha

  • Onetsetsani kuti malo osungiramo mbewu akhale a ukhondo, otetezedwa ku mbewa ndi mbalame. Denga likhale losadontha kukamagwa mvula, losaphwanyika paliponse komanso lotetezeka.

Share this Doc