ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

KASANKHIDWE KA MBEWU

KASANKHIDWE KA MBEWU

Pali mitundu ingapo ya nandolo yovomerezeka m’Malawi imene mulimi akhoza kusakhapo: yocha nsange, pakatikati komanso mochedwerapo.

Yocha Mwamsanga

  • Imacha pakati pa masiku 120 ndi 150
  • Imalola madera ambiri m’Malawi muno
  • Imafunika kupopera katatu ikayamba maluwa poteteza ku tizilombo.

ICPL 87105

(Source: Guide for Groundnut,Pigeon peas, Sorghum and Finger Millet in Malawi)

  • Imalola madera ambiri m’Malawi muno ndipo imacha pa masiku 126 basi
  • Imatalika 130 cm
  • Ndi yamaso akuluakulu ndipo imabereka matumba 16 a 50 kilogalamu pa ekala
  • Sigwidwa ndi chiwawu kawirikawiri chifukwa imacha msanga.

    ICPL 93026

(Source-Guide for Groundnut,Pigeon peas, Sorghum and Finger Millet in Malawi)

  • Imalola madera ambiri m’Malawi muno ndipo imacha pa masiku 127 basi
  • Imakula (137cm) motalikirapo kuyerekeza ndi ICPL87105
  • Ndi yamaso akuluakulu ndipo imabereka matumba 16 a 50 Kilogalamu pa ekala.

Yocha Mwapakatikati

Imacha pakati pa masiku 150 ndi 180 ndipo imalola bwino malo okwererako pang`ono.

    Mwaiwathu Alimi (ICEAP 00557)

Photo credit -Chitedze

  • Mbewu iyi imacha mwapakatikati, pa masiku 159 – 180.
  • Yopirira ku matenda a chiwawu ndi matenda ena a munthaka.
  • Mbewu yake imakhala ikuluikulu komanso imawoneka yoyererako pang’ono
  • Yamaso akuluakulu ndipo imabereka pafupifupi matumba 16 a 50 kilogalamu pa ekala imodzi.

    Chitedze 1 (Mthawajuni)

Photo credit –Chitedze RS

  • Imacha mwa pakatikati, masiku apakati pa 151 ndi 190
  • Imalola madera ambiri m’Malawi muno
  • Imachita bwino kwambiri mukayisiya kuti igonere
  • Imapilira ku matenda ena koma imatha kugwidwa ndi matenda a chiwawu
  • Imabereka pakati pa matumba 20-24 a 50 kilogalamu pa ekala.
  • Yofunika kwambiri ku misika yakunja chifukwa simavuta kusenda khungu lake.

    Chitedze 2

Photo credit –Chitedze RS

  • Imacha mwa pakatikati, masiku pakati pa 151 ndi 190
  • Imalola madera ambiri m’Malawi muno
  • Imachita bwino kwambiri mukayisiya kuti igonere
  • Imapilira ku matenda ena koma imagwidwa ndi matenda a chiwawu
  • Mbewu imakhala ikuluikulu ndipo Imabereka pakati pa matumba 20-25 a 50 kilogalamu pa ekala
  • Yofunika kwambiri ku misika yakunja.

Yocha mochedwa

    Sauma (ICPL 9145 )

(Source-Guide for Groundnut,Pigeon peas, Sorghum and Finger Millet in Malawi)

  • Iyi ndi mbewu yocha mochedwa pakati pa masiku 220 ndi 270
  • Yopirira ku matenda a chiwawu ndi nthomba
  • Mbewu iyi imakhala ndi maso akuluakulu komanso imabereka pafupifupi matumba 20 olemera 50 kilogalamu pa ekala ngati yalimidwa payokha
  • Mbewu iyi imachitanso bwino ngakhale kuibzala ndi mbewu zina.

Kachangu (ICEAP0040)

(Source-Guide for Groundnut,Pigeon peas, Sorghum and Finger Millet in Malawi)

  • Mbewu iyi imacha mochedwerako pakati pa masiku 190 ndi 240.
  • Yopirira ku matenda a chiwawu
  • Yamaso akuluakulu, yobereka kufika matumba 14 a 50 kilogalamu pa ekala ngati yalimidwa payokha.
  • Imachitanso bwino kuibzala mophatikiza ndi mbewu zina.
Share this Doc