ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

KUBZALA

KUBZALA

  • Alimi akulimbikitsidwa kubzala mbewu yovomelezeka
  • Bzalani mbewu yanu ndi mvula yoyamba kapena pamene mbewu inayo yamera (ngati mukubzala mophatikiza ndi mbewu ina)
  • Kutalikirana kwa mapando kumatengera mtundu wa mbewu yomwe mukubzala kapenso kalimidwe kake.

Mbewu yocha msanga

  • Imakhala bwino ngati yabzalidwa payokha
  • Bzalani pa mizere yotalikirana 75cm kapena 90cm
  • Mutha kubzala mikwaso iwiri kapena umodzi pa mzere umodzi.
  • Ngati mwabzala mkwaso umodzi pa mzere bzalani mbewu ziwiri pa phando pa mpata wa 20cm.
  • Ngati mwabzala mikwaso iwiri pa mzere, mikwaso italikirane 30cm ndipo mubzale mbewu imodzi pa mpata wa 10cm.
  • Mbewu ikhale yochuluka pakati pa 7 ndi 10 Kilogalamu pa ekala imodzi
  • Mungathe kubzala nandolo ocha msangayu ndi chimanga m’njira yobzala pa mizere yosiyana monga nandolo mzere umodzi chimanga mizere iwiri/itatu. 

Nandolo Ocha Mwapakatikati Ndi Ocha Mochedwa

  • Bzalani mbewu ziwiri pa phando. Mapando atalikirane 60cm pa mizere yotalikirana 75cm kapena 90cm

Kuchuluka kwa mbewu kukhale 3.33kg pa ekala imodzi. (8 Kilogalamu pa hekitala).

Kubzala Nandolo Mophatikiza Ndi Mbewu Zina

  • Nandolo amatha kubzalidwa mophatikiza ndi mbewu zina
  • Kubzalidwe kameneka nandolo amakula ‘pang’onopang’ono kwa miyezi iwiri yoyambirira ndipo amayamba kukula mofulumira pamene mbewu inayo ikayandikira kukhwima.

Zoyenera kutsatira ngati tikubzala nandolo ndi soya m’munda umodzi

Poyamba

  • Bzalani soya poyambirira. Onetsetsani kuti mizere isakhale yotalikirana kuposera 75cm
  • Bzalani soya motalikitsa 5-8cm m’mayenje ozama 3cm pa mikwaso iwiri pa mzere umodzi
  • Bzalani soya ndi mvula yoyambirira.

Kachiwiri

  • Bzalani nandolo tsiku lomwelo mwabzala mbewu ya soya
  • Bzalani mbeu zitatu pa mpata wa 90cm mu mizere yomwe mwabzalamo kale soya.
  • Onesetsani kuti mwabzala pakatikati pa mzere
  • Kubzala kotere kumafuna mbewu ya nandolo yokwana 3.33 kilogalamu pa ekala.

Zoyenera Kuchita Pamene Mukubzala Nandolo Mophatikiza Ndi Mtedza

Poyamba

  • Bzalani mtedza poyambirira ndi mvula yoyamba.
  • Dziwani kuti kuchedwatsa kubzala mtedza ndi mvula yoyambirira ndi chiyambi chopeza zokolola zochepa.
  • Mizera italikirane pa mipata ya 75cm.
  • Pangani mikwaso iwiri pa mzera yozama 5-8cm
  • Bzalani mtedza pa mipata ya 10-15cm pa mkwaso uli onse
  • Kuchuluka kwa mbeu ya mtedza umene mungafune ndi 32-40 kilogalamu pa ekala (80-100 Kilogalamu pa hekitala).

Kachiwiri

  • Bzalani nandolo tsiku lomwelo mwabzala mtedza
  • Bzalani mbeu zitatu kapena zinai pa mapando otalikirana 90cm pa mizere yomwe mwabzalamo kale mtedza
  • Nandolo abzalidwe pakati penipeni pa mzere wa mtedza
  • Kabzalidwe kotere kamafuna mbeu ya nandolo yochuluka 3.33 kilogalamu pa ekala (8Kg pa hekitala imodzi )
  • Mtedza umakumbidwa msanga ndipo nandolo amatsalira
  • Ubwino wa kabzalidwe aka ndiwakuti mbeu yachimanga ikadzabzalidwa chaka chotsatiracho imadzabereka bwino chifukwa cha chonde chochokera ku masamba a nandolo.

Zoyenera Kuchita Pamene Mukubzala Nandolo Mophatikiza Ndi chimanga

  • Limani nandolo wocha mwasanga mophatikizana ndi chimanga
  • Mutha kuphatikiza nandolo ndi chimanga motere
  • Pobzala chimanga ndi nandolo pa mzere umodzi kapena
  • Pobzala chimanga chokha pa mizere motsatana ndi mizere ya nandolo yekhanso iwiri kapena ingapo.

Poyamba

  • Mizere ya chimanga italikirane pa mipata ya 75cm
  • Bzalani chimanga ndi mvula yoyamba
  • Bzalani chimanga chimodzi pa phando motalikirana 25cm.

Kachiwiri

  • Bzalani nandolo 3-4 pa phando motalikirana 90cm pa mizere yomwe mwabzala kale chimanga (patatha masabata awiri chimanga chitabzalidwa)
  • Kapena kubzala nandolo 3-4 pa phando motalikirana 90cm pa mizere iwiri kapena ingapo ya nandolo yekhayekha motsatana ndi mizere ya chimanga.
Share this Doc