KUKOLOLA NDI KUOMBA NANDOLO
KUKOLOLA NDI KUOMBA NANDOLO
- Kololani nandolo pamene wakhwima ndikuyamba kuuma
- Kololani nandolo nthawi ya m’mawa kuopa kuthetheka
- Nandolo yemwe wacha amaoneka ndi makoko owuma
- Nandolo angathe kukololedwa podula mitengo yake ndikumanga kupititsa malo amene tikaombere
- Komanso nandolo angathe kukololedwa populula yekhayo wauma ndi kupititsa pa malo pomwe tikaombere. Njira iyiyi imathandiza kuti nandolo adzachitenso maluwa chaka chinacho ndi kudzaberekanso
- Ombani nandolo ndi timitengo ting’onoting’ono pa phasa / tenti / lona
- Petani nandolo wanu kuchotsa zinyalala, miyala komanso nandolo osakhwima.