KUSANKHA MALO OLIMAPO NANDOLO
KUSANKHA MALO OLIMAPO NANDOLO
- Sankhani malo a dothi la chonde komanso lotaya madzi
- Nandolo samachita bwino pa malo a lowe
- Pewani kubzala nandolo malo a chipalawe (a dothi la mchere) chifukwa nandolo sachita bwino.
KUKONZA M’MUNDA
- Tipulani/gaulani m’munda mwanu bwino kuti musunge nthaka ndi chinyontho
- Thirani manyowa m’munda pa milungu iwiri kapena inayi nthawi yobzala isanafike
- Pangani mizere yotalikirana 75cm kapena 90cm.