MAU OYAMBA
ULIMI MA NANDOLO
Photo credit -Chitedze Reserch Station
MAU OYAMBA
- Nandolo ndi mbewu ya m’gulu la nyemba yomwe imalimidwa kwambiri ndi alimi ang’onoang’ono maka kumwera kwa dziko la Malawi ngati chakudya komanso kugulitsa konkuno kapenanso mayiko akunja
- Amakoloredwa mochedwa kusiyana ndi mbeu zina za mu gulu la nyemba
- Nandolo amakhoza kulimidwa payekha m’munda komanso mophatikiza ndi mbewu zina monga chimanga, mtedza, thonje, mapira komanso soya
- Ndi imodzi mwa mbewu zomwe sizifuna ndalama kapena zipangizo zambiri pa ulimi wake
- Nandolo ali ndi mitsitsi/mizu yaitali yomwe imapita pansi kwambiri motero amatha kupirira ku ng’amba za kanthawi kochepa.