TIZIROMBO NDI MATENDA OWONONGA NANDOLO
TIZIROMBO NDI MATENDA OWONONGA NANDOLO
Tizirombo
- Tizirombo todya masamba komanso toboola nandolo pamene ali wamuwisi tingathe kuchepetsa zokolola ndi magawo asanu ndi awiri mwa magawo khumi (70%)
- Akafadala a mu nandolo amaononga kwambiri maluwa a nandolo ndikuchepetsa zokolola kwambiri
- Kunena motsindika nandolo yense wocha msanga akuyenera kupoperedwa kawiri nthawi ya maluwa komanso kawiri nthawi yomwe nandolo wabereka pofuna kuthana ndi tizirombo towononga.
Tsatani ndondomeko ili m’munsiyi pothana nd tizirombo.
Tizirombo tina towononga nandolo
Nsabwe
Mphutsi zoyera za mdothi
Mbozi
Ziwala – Nunkadala
Adults of blister beetle (Gonondo)
Matenda Komanso Kuthana Nawo Kwake
Matenda ofota (Fusarium wilt)
- Matenda ovutirapo ndipo amachukira kuno ku Malawi
- Amayamba kugwira mizu kenako kufalikira mtengo wonse
- Masamba amasanduka a chikasu kenako kuuma ndi kugwa
- Tsinde la mtengo wa nandolo likhala loderadera kenako kuderatu ndi kuuma.
Kupewa ndi kuteteza kumatendawa
- Bzalani mbewu yopirira ku matendawa ngati Sauma kapena Kachangu komanso yopanda matendawa
- Kuzula ndi kutentha mbewu zonse za matendewa
- Kubzala nandolo ku munda umene ulibe mbiri ya matendawa
- Kubzala mbewu mwakasinthasintha.
(Source-NCIPM)
Nthomba (Cecospora leafspot)
- Matendawa amachulukira kumalo a chifunga ngati nyengo ya mvula yatalika
- Imatha kuchepetsa zokolola mpaka 85% ngati masamba ayoyoka nthawi ya maluwa komanso kubala kusanafike
- Masamba okhwima amaonetsa madothomadotho (spots) odera amaonekwedwe osiyanasiyana
- Matendawa akapitirira madothomadotho amakumana ndipo masamba amayoyoka
- Kukumana kwa madothomadothoku kumathanso kuoneka pa nthambi zing’onozing’ono ndikupangitsa kuti songa za nthambizo ziume ndi kuferatu.
Kupewa ndi kuteteza kumatendawa pobzala
- Bzalani mbewu yanu kutali ndikomwe nandolo amakonda kulimidwa
- Bzalani mbewu yopirira ku matendawa
- Kuzula ndi kutentha mbewu zonse za matendewa
- Kubzala mbewu mwakasinthasintha
- Kupopera nandolo ndi makhwala achiwawu ngati a benomyl kapena mancozeb.
Cercospora spots on leaves (Source-Handbook for Pigeon pea Diseases)
Cercospora spots on flowers (Source-NCIPM)
Chiwawu (Powdery mildew)
- Matendawa ndi osavuta kwambiri ndipo amatha kupezeka m’madera ena kuno ku Malawi
- Amapezeka ku madera komwe nandolo amalimidwa kwambiri ngati nyengo ya mvula ipitirira
- Poyambirira pamwamba pa masamba pamaoneka madonthomadotho
- Kunsi kwa masamba amunsi kumakhala madontho oyera amene amafalikira kumasamba ang’onoang’ono mpakana mtengo wonse wa nandolo umatuwa ngakhalenso maluwa ndi zibalo
- Mukhoza kupewa ndi kuteteza nandolo ku matendawa pobzala mbewu yopirira ku matendawa ngati Sauma kapena Kachangu, kubzala mbewu moyambirira komansokubzala mbewu mwakasinthasintha.
(Source-Handbook for Pigeon pea Diseases)