ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

KABZALIDWE

KABZALIDWE

Mizere italikirane masentimita 75. Mikwasa italikirane pakati pa masentimita 20 ndi 30. Mapando atalikirane masentimita 5 ndipo phando lizame masentimita 2.5.

Kubzala popanda mizere (pongotipulidwa) mikwasa italikirane masentimita 45 ndipo mapando atalikirane masentimita 5 ndipo bzalani mbeu imodzi pa phando kapena mbeu ziwiri pa mapando otalikirana masentimita 10.

Bzalani makilogalamu 24-32 pa ekala soya mng’onong’ono kapena makilogalamu 32-40 pa ekala soya mkulumkulu.

Mitundu ya soya

Mitundu ya soya ndi monga Makwacha, Nasoko, Tikolole ndi Serenade. Tikolole safunika inokalanti. Mukalima motsatira ndondomeko mumatha kukolola pakati pa makilogalamu 1000 ndi 1200 pa ekala imodzi.

Kuti mudziwe za mtundu wasoya womwe mungabzale m’dera lanu kafunseni ku Ofesi ya za Malimidwe m’dera lanu.

Share this Doc