ZAULIMI APP

ZAULIMI APP

Making Agricultural Extension Services Easily Available

Docy

KASUNGIDWE KA SOYA

KASUNGIDWE KA SOYA

  • Sungani zokolola zanu pa malo abwino opanda chinyezi, opita mphepo bwino, otetezedwa ku mbewa komanso osadontha madzi.
  • Soya amasungika bwino mukamuika mu matumba a 50 kilogalamu.
  • Konzani thandala kuti asakhale pansi komanso onetsetsani kuti asakhudze khoma posiya mpata m’phepete mwa khoma ndipo mpatawu ukhale okuti munthu atha kumazungulira m’mbali mwake, choncho mphepo imadutsa bwino mbali zonse kupangitsa kuteteza kuonongeka kwa zokolora zanu.

storage- soya

 Malo abwino osungiramo soya

Mkati komanso kunja kuzungulira malo osungiramo mbewu akhale a ukhondo, otetezedwa ku mbewa ndi mbalame. Denga likhale losadontha komanso lotetezeka.

Share this Doc