KUSUNGA CHIMANGA
KUSUNGA CHIMANGA
Chimanga chimasungidwa bwino mukayika mu nkhokwe kapena mumatumba a ma kilogalamu 50. Chapani matumba m’madzi otentha musanayikemo chimanga chanu ngati matumbawo anagwiritsidwapo ntchito kale.
Ikani matabwa kapena mitengo ndipo matumba akhale pamwamba asakhudze pansi kapena khoma kuti mpweya udzitha kudutsa bwino komanso kupewa chinyenzi.
Onetsetsani kuti malo osungiramo mbewu akhale a ukhondo, otetezedwa ku makoswe ndi mbalame. Denga likhale losadontha kukamagwa mvula, losaphwanyika paliponse komanso lotetezeka.