KUBZALA
KUBZALA
Bzalani soya wa m’mvula pakati pa miyezi ya Novembala ndi Desembala ndipo wothirira mubzale pakati pa miyezi ya Meyi ndi Juni.
Bzalani mbewu chinyontho chikakhala chokwanira mvula ikangogwa.
Kuthira Inokulanti mu Mbewu ya Soya
Thirani inokulanti mu mbewu ya soya musanabzale kuti mchere okulitsa mbewu ochuluke m’nthaka.Tsatirani malangizo a kathiridwe ka inokulanti kuti inokulantiyo agwire ntchito moyenera. Gulani inokulanti ku ma ofesi a kafukufuku a unduna wa boma komanso kwa ma agulodila ovomerezeka.
Kuthira mankhwala oteteza mbewu
Thirani mankhwala a Thiram ku mbewu ya soya omwe amateteza mbewuyi ku matenda ochokera mu nthaka. Werengani malangizo a kathiridwe ka mankhwalawa omwe amalembedwa kunja kwa paketi.