KUKOLOLA
KUKOLOLA
- Kololani soya pamene wakhwima pakatha masiku 100 mpaka 140 kuchokera tsiku lomwe munabzala potengera mtundu wambewu
- Kololani pamene soya wambiri wauma
- Soya wowuma amachita phokoso mukamgwedeza.
- Kololani soya kum’mawa kuopetsa kuti angathethekere m’munda
- Musakolore ngati kwagwa mvula kuti musavutike ndi kuumitsa soya wanu.
- Pamene mukukolora, dulani soya patsinde pogwiritsa ntchito chisikiro kapena chikwakwa. Onetsetsani kuti mizu ya soya yatsalira m’nthaka kuti ithandize kuwonjezera chonde.
- Nyamulani soya mosamala kukayika pa malo owombera
- Wombani soya ndi manja kapena makina pamene wauma bwino.
- Wombani ndi timitengo ting’onoting’ono kuopetsa kuswa soya.
- Mungathe kukolora matumba 16 mpaka 20 a soya wolemera makilogalamu 50 pa ekala.