KUTETEZA KU TIZILOMBO NDI MATENDA
KUTETEZA KU TIZILOMBO NDI MATENDA
Soya amagwidwa ndi matenda komanso amaonongeka ndi tizirombo tosiyanasiyana monga mbozi ndi chiswe.
TIZILOMBO
Mbozi
Zilipo zosiyanasiyana zomwe zimaboola ndi kudya masamba, maluwa komanso zitheba za soya. Poperani Carbaryl kapena Cypermethrin kusakaniza ndi Dimethoate 10EC kuti muphe mbozi zimenezi.
Mbozi
Chiswe
Chimawononga soya pamsinkhu uliwonse makamaka kukachita ng’amba. Chitani kasinthasintha wa mbewu kuti muchepetse vuto la chiswe; kapena poperani chlorpyrifos kuti muphe chiswe.
Chiswe