MATENDA
MATENDA
Dzimbiri / Chiwawu
Dzimbiri / Chiwawu ndi matenda amene amawononga masamba a soya ndipo amathothoka akadali anthete ndi kuchepetsa zokolola koposa theka.
Dzimbiri / Chiwawu
Kuteteza ku Dzimbiri
- Bzalani mofulumira mitundu ya soya yovomerezeka komanso yopilira ku matenda.
- Zulani udzu ndi mbewu zomera zokha ndikuotcha mbewu zonse zomwe zagwidwa ndi matendawa.
Kuteteza ku matenda onse
- Musabzale mbewu zosweka chifukwa ndi momwe tizilombo timapezera mpata kulowera mumbewuyi ndikufalitsa matenda amene timayambitsa.
- M’munda mukhale mwa ukhondo
- Bzalani mwakasinthasintha ndi chimanga kapena mawere
- Bzalani moyambilira
- Thirani mankhwala kuti muthane ndi dzimbiri. Kuti mudziwe zambiri za tizirombo komanso matenda owononga soya kafunseni ku Ofesi ya za malimidwe m’dera lanu.