CryptApp

KUSANKHA MALO NDI ZIPANGIZO ZOMANGIRA KHOLA

KUSANKHA MALO NDI ZIPANGIZO ZOMANGIRA KHOLA

  • Sankhani malo otetezedwa ku mbava ndi nyama zolusa
  • Malo omanga khola akhale mbali yomwe ikupita mphepo kupewa fungo kuti lisalowe mnyumba yogona
  • Mangani malo opanda lowe
  • Khola lisatalikire kwambiri kuchokera pa nyumba yogona anthu
  • Lambulani tchire lonse kuzungulira khola malo okwana mamita atatu kuopetsa zirombo zogwila nkhuku.

Zipangizo zomangira Khola

Gwiritsani ntchito zipangizo zomangira khola zopezeka mosavuta monga:

  • Mitengo
  • Njerwa
  • Bango
  • Dothi
  • Udzu, malata ndi zina zotero.
Share this Doc
CONTENTS